Luke 7:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Panali anthu aŵiri amene adaakongola ndalama kwa munthu wokongoza ndalama. Wina adaakongola ndalama makumi asanu, wina ndalama zisanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ace a marupiya mazana asanu, koma mnzace makumi asanu.