Luke 7:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero, Yesu adacheukira mai uja, nauza Simoni kuti, “Ukumuwona maiyu? Ine ndaloŵa m'nyumba mwako muno, iwe sudandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma iyeyu wakhala akukhetsera misozi pa mapazi anga, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene iye anaceukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lace.