Luke 7:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, ndinena kwa iwe, Macimo ace, ndiwo ambiri, akhululukidwa; cifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.