Luke 7:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita’, amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera’, amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti’, amachitadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akuru anga, ndiri nao asilikari akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tacita ici, nacita.