Luke 8:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho ayang'ane, koma asapenye, ndipo amve, koma asamvetse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse,