Luke 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nacotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.