Luke 8:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo palibe munthu, atayatsa, nyali, aibvundikira ndi cotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pacoikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.