Luke 8:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso azimai ena amene Yesu adaaŵatulutsa mizimu yoipa ndi kuŵachiza nthenda zina. Azimaiwo ndi aŵa: Maria, wotchedwa Magadalena, (amene mwa iye mudaatuluka mizimu yoipa isanu ndi iŵiri);
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi akazi ena amene anaciritsidwa mizimu yoipa ndi nthenda zao, ndiwo, Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinaturuka mwa iye,