Luke 8:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu adafika pa mtunda, munthu wina wochokera ku mudzi wakomweko, adadzakumana naye. Munthuyo adaali ndi mizimu yoipa, ndipo kuyambira kale sankavalanso zovala. Sankakhala m'nyumba, koma ku manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ataturuka pamtanda iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanabvala cobvala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.