Luke 8:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Yohana, mkazi wace wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi eumacao.