Luke 8:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ziwandazo zinaturuka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.