Luke 8:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu onse a ku malo ozungulira Geregesa adapempha Yesu kuti achoke kumeneko, chifukwa iwo anali ndi mantha aakulu. Choncho Yesu adaloŵa m'chombo, nkumabwerera ku tsidya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha akulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa Ioyandikira anamfunsa iye acoke kwa iwo; cifukwa anagwidwa ndi mantha akuru. Ndipo iye analowa m'ngalawa, nabwerera.