Luke 8:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wace zonse, ndipo sanathe kuciritsidwa ndi mmodzi yense,