Luke 8:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.