Luke 8:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu akulankhulabe, kudafika munthu wina kuchokera kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mene iye anali cilankhulire, anadza wina wocokera kwa mkuru wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usambvute Mphunzitsi.