Luke 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira. Zidapondedwa, ndipo mbalame zidazitolatola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaturuka wofesa kukafesa mbeu zace; ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.