Luke 8:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufika iye kunyumbako, sanaloleza wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amace.