Luke 8:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse ankalira ndi kubuma. Koma Yesu adati, “Musalire, mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse analikumlirira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudzigugudapacifuwa. Koma iye anati, Musalire; pakuti iye sanafa, koma agona tulo.