Luke 9:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene atumwi aja adabwerako, adafotokozera Yesu zonse zimene adaachita. Tsono Iye adaŵatenga nakakhala nawo paokha ku mudzi wina, dzina lake Betsaida.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumudzi dzina lake Betsaida.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera iye zonse anazicita. Ndipo iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka ku mudzi dzina lace Betsaida.