Luke 9:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, naciritsa amene anasowa kuciritsidwa.