Luke 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumilaga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite ku midzi yoyandikira ndi kumiraga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; cifukwa tiri ku malo acipululu kuno.