Luke 9:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.” Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.