Luke 9:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Auzeni anthuŵa akhale pansi m'magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000). Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma iye anati kwa ophunzira ace, Khalitsani iwo pansi magulu magulu, ngati makumi asanu asanu.