Luke 9:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu munthu akamakana Ine ndiponso mau anga, nanenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamene ndidzabwera ndili ndi ulemerero wanga ndi wa Atate anga, ndi wa angelo oyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti amene ali yense: adzacita manyazi cifukwa ca Ine ndi mau anga, Mwana wa munthu adzacita manyazi cifukwa ca iye, pamene adzafika ndi ulemerero wace ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.