Luke 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵauza kuti, “Musatenge kanthu pa ulendowu. Musatenge ndodo, kapena thumba lapaulendo, kapena kamba kapena ndalama. Musakhale ndi mikanjo iŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndarama; ndipo musakhale nao malaya awiri.