Luke 9:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m'tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu aŵiri aja ali naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wace, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi iye.