Luke 9:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mauwo atamveka choncho, ophunzira aja adaona kuti Yesu ali yekha. Iwo adangokhala chete masiku amenewo, osauza wina aliyense zimene adaaziwonazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala cete, ndipo sanauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.