Luke 9:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina pakati pa anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Aphunzitsi, chonde tandiwonerani mwana wangayu, ine mwana ndi mmodzi yemweyu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, anafuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, anapfuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; cifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine: