Luke 9:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu onse aja adazizwa nazo mphamvu za Mulunguzi. Pamene anthu onse aja ankazizwabe ndi zonse zimene Yesu adaachita, Iye adauza ophunzira ake kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu. Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onse anadabwa pa ukulu wace wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazicita, iye anati kwa ophunzira ace,