Luke 9:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaadziŵa zimene zinali kukhosi kwao. Tsono adatenga mwana, namukhazika pambali pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,