Luke 9:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yohane adati, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa, chifukwa sayenda nafe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.