Luke 9:57 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo anali panjira, munthu wina adauza Yesu kuti, “Ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa iye, Ine ndidzakutsatani kumene kuli konse mukapitako.