Luke 9:59 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yesu adauza munthu wina kuti, “Iwe, unditsate!” Iyeyo adati, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga.