Malachi 1:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kudakakhala bwino kwambiri kuti wina mwa inu atsekeretu zitseko za Nyumba yanga, kuti mungayatse moto pachabe pa guwa langa. Sindikukondwera nanu, sindidzazilandira zopereka zanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto cabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira capereka m'dzanja lanu.