Malachi 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunenanso kuti, “Inu mumati, ‘Ha, kutopetsa zimenezi!’ Kenakanso nkumandinyodola. Mumabwera ndi nyama zakuba kapena zopunduka kapena zodwala ngati nsembe zanu, kodi Ine ndidzazilandira?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukutinso, Taonani, ncolemetsa ici! ndipo mwacipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.