Malachi 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina Aedomu adzanena kuti, “Mulungu adapasula nyumba zathu, komabe ife tidzazimanganso.” Koma Chauta Wamphamvuzonse adzati, “Alekeni amangenso, Ine ndidzazigwetsanso. Anthu adzalitchula dziko loipa, la anthu amene Chauta adaŵatemberera mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.” Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawacha, Dziko la coipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao cikwiyire.