Malachi 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mwana amapatsa ulemu bambo wake ndipo kapolo amaopa mbuye wake. Ngati Ine ndine bambo wanu, nanga ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiwopa kuli kuti, Ansembe inu, amene mumanyoza dzina langa. Komabe mumanena kuti, kodi dzina lanu timalinyoza bwanji?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana alemekeza atate wace, ndi mnyamata mbuye wace; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?