Malachi 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mukaperekera nsembe nyama zakhungu, kodi si cholakwa? Mukaperekera nsembe nyama zopunduka kapena zodwala, kodi si cholakwa? Bwanamkubwa wanu mutampatsa mphatso zotero, kodi angazilandire? Kodi inuyo angakukomereni mtima?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe coipa! ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe coipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? kapena adzakubvomerezani kodi? ati Yehova wa makamu.