Malachi 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Yuda akhala osakhulupirika, ku Israele ndi ku Yerusalemu akhala akuchita zinthu zonyansa. Anthu a ku Yuda aipitsa Nyumba ya Chauta imene Iye amaikonda. Akhala akukwatira akazi opembedza milungu yachikunja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yuda wachita monyenga, ndi m'Israele ndi m'Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yuda wacha monyenga, ndi m'Israyeli ndi m'Yerusalemu mwacitika conyansa; pakuti Yuda waipsa cipatuliko ca Yehova cimene acikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mlungu wacilendo.