Malachi 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zina zimene mumachita ndi izi: mumadandaula ndi kulira kwambiri mpaka kukhathamiza guwa la Chauta ndi misozi, chifukwa Iye amakana kuyang'ana nsembe zanu, osafuna kulandira mphatso iliyonse yodzatula inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ici mubwereza kucicita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso copereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.