Malachi 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukuti, Cifukwa ninji? Cifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamcitira cosakhulupirika, cinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.