Malachi 2:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi suja Mulungu adakulenga, iwe ndi mkazi wako, kukhala mmodzi, thupi ndi mzimu womwe? Nanga pakutero Mulunguyo ankafuna chiyani? Ankafunatu ana ompembedza Iye. Motero samala moyo wako ndipo khala wokhulupirika kwa mkazi wako woyamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamcitire monyenga mkazi wa ubwana wace ndi mmodziyense.