Malachi 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi iye wakukuta cobvala cace ndi ciwawa, ati Yehova wa makamu; cifukwa cace sungani mzimu wanu kuti musacite mosakhulupirika.