Malachi 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwatopetsa Chauta ndi zolankhula zanu. Komabe mumati, “Kodi tamtopetsa bwanji?” Mwamtopetsa ponena kuti, “Aliyense wochita zoipa ndi wabwino pamaso pa Chauta, ndipo Iye amakondwera naye.” Kapenanso pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wochita zolungamayo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu. Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?” Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi ciani? Ndi ici cakuti munena, Yense wakucita coipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa ciweruzo?