Malachi 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mudzadziŵa kuti ndakupatsani lamulo ili kuti chipangano changa ndi ansembe, zidzukulu za Levi, chisaphwanyike. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti cipangano canga cikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.