Malachi 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapangana nawo chipangano chopatsa moyo ndi mtendere. Ndidaŵapatsa zimenezi kuti azindiwopa, ndipo adandiwopadi namalemekeza dzina langa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cipangano canga cinali naye ca moyo ndi ca mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa cifukwa ca dzina langa.