Malachi 2:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malangizo amene ankapereka anali oona, pakamwa pao sipankatuluka zosalungama. Ankamvana nane, ndipo ankayenda mokhulupirika ndi Ine, motero ankabweza anthu ambiri m'njira zao zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeka m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cilamulo ca zoona cinali m'kamwa mwace, ndi cosalungama sicinapezeka m'milomo mwace; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu,