Malachi 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pajatu ndi ntchito ya ansembe kuphunzitsa nzeru zoona za Mulungu, anthu ayenera kupita kwa iwo kuti akaphunzire zimene Ine ndifuna, chifukwa ansembewo ndiwo amithenga a Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga cidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna cilamulo pakamwa pace; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.