Malachi 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu ansembe mudasiya njira yanga. Mudaphunthwitsa anthu ambiri ndi zophunzitsa zanu. Mudaipitsa chipangano changa ndi Alevi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mwapambuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'cilamulo; mwaipsa cipangano ca Levi, ati Yehova wa makamu.