Malachi 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Inenso ndakusandutsani onyozeka ndi achabechabe pamaso pa anthu, popeza kuti simudatsate njira zanga, ndipo mwakhala mukukondera poweruza milandu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Inenso ndakuikani onyozeka ndi ocepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pocita cilamulo.